Bwalo la milandu ku Nkhotakota lagamula bambo wa zaka 35 a Anthony Phiri kukakhala ku ndende kwa zaka zinayi popezeka ndi mlandu wothawa komanso kumusiya yekha mwana wobala okha.
Mkulu woimira boma pa milandu a Thokozani Juziwel adauza bwalo kuti bamboyu adakwatira mayi Vester Nyoni m’chaka cha 2023, ndipo banja lidatha mwanayo atabadwa ndipo ali ndi mwezi umodzi chifukwa cha khalidwe lawo loipa.
Kutsatira kusiyana komwe kudachitika, a Phiri adapita ku Mozambique ndipo abwerako chaka chino, ndipo pa 12 September 2025 adapita ku mudzi kwa mkazi wawo wakaleyu ku Buwa ndikutenga mwanayo opanda chilolezo.
“Choncho pa 20 September 2025, bambowa anamusiya yekha mwanayu pa tchire komanso malo omwe ali oophya kwambiri a Kaombe komwe anthu odutsa anapeza mwanayu akulira yekha pakati pa usiku.” Iwo adatero.
Pa nthawi yomwe mayi komanso achibale a mwanayu anapezeka, anakasiya nkhaniyi ku polisi omwe adamanga Anthony Phiri.
Pomwe iwo adawonekera ku bwalo la mlandu, a Phiri adaukana mlanduwu, ndipo boma linabweretsa mboni zake zitatu zomwe zinafotokoza za nkhaniyi.
Kenako, a Phiri adapempha bwalo kuti liwamvere chisoni chifukwa anachita izi kaamba ka mowa womwe iwo adalawako pa nthawiyo, ndipo achita chotheka kuti asamalira mwanayo, bwalo likawapatsa mwayi wina.
Komabe, woyimira boma a Juziwel adauza wozenga mlanduwu kuti bambo Phiri akuyenera kulandira chilango chokhwima kuti ena omwe angakhale ndi nzeru ngati izi asachite.
Ndipo popereka gamulo wozenga mlandu a Violet Dzimbiri adagwirizana ndi ganizo la boma ndipo adagamula a Phiri kukakhala ku ndende kwa zaka zinayi.
Anthony Phiri amachokera m’mudzi mwa Chimtali village TA Chitseka m’boma la Lilongwe.