Pali chiopsezo kuti chiwerengero cha achinyamata ozungilira mitu chitha kukwera kwambiri kudera la Chemusa munzinda wa Blantyre komwe akuti mchitidwe osuta bositiki omatira zinthu komaso miyala ya m’buka wafika posauzana.
Fred Msiyambiri yemwe ndi khansala wa wadi ya Mussa-Magasa anadandaula zakukula kwa mchitidwewu pa maliro ena mderali Lachitatu sabata ino, komwe anachonderera achinyamata kuti asiye.
Titamukokera pambali kuti afotokoze bwino za nkhaniyi, Msiyambiri wati achinyamata angapo mderali asokonekera mitu kamba ka khalidweli zomwe wati ndichitsimikizo choti mchitidwewu ndioopsa.
“Achinyamata angapo mitu yawo siikugwira. Wina mpaka anawagwira mayi ake pakhosi moti panopa mayi akewo akumakhala moopa, pena zikumafika mpaka poti akumagona mchimbudzi. Ndizovetsa chisoni kuti atsikanaso akupanga nawo khalidweli,” watelo Msiyambiri.
Msiyambiri wati achinyamatawa akasuta m’buka kapena bositiki, akumatha masiku atatu osamva njala komaso osagona tulo, ndipo watiso masiku atatu akatha, bositikiyu akayamba kusungunuka m’mutumo, osutawo akumathaso masiku ena atatu osamva njala komaso osagona.
Msiyamiri: achinyamata ena asokonekera mitu
“Ambiri zikuwapengetsa, ena akumakhala ngati mavampaya, mpaka kumavutitsa ndikuopseza makolo,” watelo Msiyambiri. “Panopa tagwetsa nyumba ziwiri zomwe achinyamata amenewa amagwiritsa ntchito kumachitira mchitidwe umenewu.”
Iye wati pano adindo mderali akukoza misonkhano yoyimayima kuti afalitse zakuipa kwa kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza ubongowa.
“Tikufuna tiwapulumutse achinyamata ndiye kutsogoloku tikhala ndi ma roadshow, komwe tikhale tikukumana ndi achinyamata amenewa kuti tiwadziwitse zakuopsa kwa mchitidwewu,” wateloso Msiyambiri.
Malingana ndi Msiyambiri, achinyamatawa akumaika miyala ya m’buka mu babu lomwe akumalilumikiza ndi payipi ya cholembera, kuyatsa ndikumasuta. Mbali inayi, bositiki akuti akumamuika mujumbo, kumukhutchumula kenaka ndikumafwenkha mpweya wakewo.